8. Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakucokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.
9. Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israyeli monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakuchera mphesa m'mitanga yace.
10. Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.
11. Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.
12. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.
13. Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita monyenga,
14. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.