Yeremiya 51:35-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Wokhala m'Ziyoni adzati, Ciwawa anandicitira ine ndi thupi langa cikhale pa Babulo; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi.

36. Cifukwa cace Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera cilango cifukwa ca iwe; ndidzaphwetsa nyanja yace, ndidzaphwetsa citsime cace.

37. Ndipo Babulo adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, cizizwitso, cotsonyetsa, wopanda okhalamo.

38. Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzacita nthulu ngati ana a mikango.

39. Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone cigonere, asanyamuke, ati Yehova.

40. Ndidzawagwetsa kuti aphedwe manga nkhosa zamphongo, ndi atonde.

41. Sesake wagwidwatul cimene dziko lonse lapansi linacitamanda calandidwa dzidzidzi Babulo wakhalatu bwinja pakati pa amitundu

Yeremiya 51