Yeremiya 51:15-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yace, ndi luso anayala thambo;

16. pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, aturutsa mphepo ya m'nyumba za cuma zace.

17. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golidi acitidwa manyazi ndi fanizo lace losema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya m'menemo.

18. Ngwacabe, ciphamaso; nthawi yakulangidwa kwao adzatayika.

19. Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndi mtundu wa colowa cace, dzina lace ndi Yehova wa makamu.

20. Iwe ndiwe cibonga canga ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzatyolatyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

21. ndi iwe ndidzatyolatyola kavalo ndi wakwera wace;

22. ndi iwe ndidzatyolatyola gareta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzatyolatyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzatyolatyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzatyolatyola mnyamata ndi namwali;

23. ndi iwe ndidzatyolatyola mbusa ndi zoweta zace; ndi iwe ndidzatyolatyola wakulima ndi gori la ng'ombe lace; ndi iwe ndidzatyolatyola akazembe ndi ziwanga,

24. Ndipo ndidzabwezera Babulo ndi okhala m'Kasidi zoipa zao zonse anazicita m'Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.

25. Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.

26. Ndipo sadzacotsa pa iwe mwala wa pangondya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

27. Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenaza; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati mandowa.

28. Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ace, ndi ziwanga zace zonse, ndi dziko lonse la ufumu wace.

29. Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babulo ziripobe, zoti ayese dziko la Babulo bwinja lopanda wokhalamo.

Yeremiya 51