13. Pakuti ndalumbira, Pali Ine, ati Yehova, kuti Boma adzakhala cizizwitso, citonzo, copasuka, ndi citemberero; ndipo midzi yace yonse idzakhala yopasuka cipasukire.
14. Ndamva mthenga wa kwa Yehoya, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.
15. Pakuti, caona, ndakuyesa iwe wamng'ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.
16. Koma za kuopsya kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa citunda, ngakhale usanja cisanja cako pamwamba penipeni ngati ciombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.