10. Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Akasidi, amene adzadza kwa ife; koma inu, sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda.
11. Comweco pamene Ayuda onse okhala m'Moabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babulo inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
12. pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.