Yeremiya 4:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efraimu:

16. Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira ku dziko lakutari, nainenera midzi ya Yuda mau ao.

17. Monga adindo a m'munda amzinga iye; cifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

18. Njira yako ndi nchito zako zinakucitira izi; ici ndico coipa cako ndithu; ciri cowawa ndithu, cifikira ku mtima wako.

19. Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga peni peni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.

20. Alalikira cipasuko cilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsaru zanga zocinga m'kamphindi.

21. Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?

Yeremiya 4