Yeremiya 32:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo nditapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,

17. Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikuru ndi mkono wanu wotambasuka; palibe cokulakani Inu;

18. a amene mucitira cifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'cifuwa ca ana ao a pambuyo pao, dzina lace ndi Mulungu wamkuru, wamphamvu, Yehova wa makamu;

19. wamkuru, m'upo, wamphamvu m'nchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa cipatso ca macitidwe ace;

20. amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, m'Israyeli ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;

21. ndipo munaturutsa anthu anu Israyeli m'dziko la Aigupto ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;

Yeremiya 32