Yeremiya 26:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akuru ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.

12. Pamenepo Yeremiya ananena kwa akuru onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mudzi uwu mau onse amene mwamva.

13. Cifukwa cace tsopano konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka coipa cimene ananenera inu.

14. Koma ine, taonani, ndiri m'manja anu; mundicitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu.

15. Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosacimwa, ndi pa mudzi uwu, ndi pa okhalamo ace; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.

Yeremiya 26