30. Cifukwa cace muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzachula mau ace mokhalamo mwace moyera; adzabangulitsira khola lace; adzapfuula, monga iwo akuponda mphesa, adzapfuulira onse okhala m'dziko lapansi.
31. Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.
32. Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.
33. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.
34. Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akuru a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati cotengera cofunika.