1. Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, mitanga iwiri ya nkhuyu yoikidwa pakhomo pa Kacisi wa Yehova; Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo atacotsa am'nsinga Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akuru a Yuda, ndi amisiri ndi acipala, kuwacotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babulo.
2. Mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kuca; ndipo mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.