1. Cimo la Yuda lalembedwa ndi peni lacitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa colembapo ca m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu.
2. Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao ku mitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitari.
3. Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka cuma cako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, cifukwa ca cimo, m'malire ako onse.