Yeremiya 16:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pamenepo uziti kwa iwo, Cifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu yina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga cilamulo canga;

12. ndipo mwacita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wace woipa, kuti musandimvere Ine;

13. cifukwa cace ndidzakuturutsani inu m'dziko muno munke ku dziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu yina usana ndi usiku, kumene sindidzacitira inu cifundo.

14. Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto.

Yeremiya 16