Yeremiya 14:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndikaturukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.

19. Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!

20. Tibvomereza, Yehova, cisalungamo cathu, ndi coipa ca makolo athu; pakuti takucimwirani Inu.

21. Musatinyoze ife, cifukwa ca dzina lanu; musanyazitse mpando wacifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.

22. Mwa zacabe za mitundu ya anthu ziripo kodi, zimene zingathe kubvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.

Yeremiya 14