Yeremiya 11:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, pamene ayesa imso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera cilango, pakuti kwa Inu ndaulula mlandu wanga.

21. Cifukwa cace atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;

22. cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao amuna ndi akazi adzafa ndi njala;

23. ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera coipa pa anthu a ku Anatoti, caka ca kulangidwa kwao.

Yeremiya 11