1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2. Imvani mau a pangano ili, nenani kwa anthu a Yuda, ndi anthu a Yerusalemu;
3. ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisrayeli: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili,
4. limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, m'ng'anjo ya citsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwacita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;
5. kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko mayenda mkaka ndi uci, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.