Rute 2:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Nati Naomi kwa mpongozi wace, Yehova amdalitse amene sanaleka kuwacitira zokoma amoyo, ndi akufa. Ndipo Naomi ananena baye, Munthuyu ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera colowa.

21. Ndipo Rute Mmoabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kuceka zanga zonse za m'minda.

22. Nati Naomi kwa Rute mpongozi wace, Ncabwino, mwana wanga, kuti uzituruka nao adzakazi ace, ndi kuti asakukomane m'munda wina uti wonse.

23. Momwemo anaumirira adzakazi a Boazi kuti atole khunkha kufikira atatha kuceka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wace.

Rute 2