Oweruza 6:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midyani zaka zisanu ndi ziwiri.

2. Pamene dzanja la Midyani linalaka Israyeli, ana a Israyeli anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga cifukwa ca Midyani.

3. Ndipo kunali, akabzala Israyeli, amakwera Amidyani, ndi Amaleki, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;

4. nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira cocirira njala m'Israyeli, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena buru.

5. Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kucuruka kwao; iwowa ndi ngamila zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.

Oweruza 6