1. NYIMBO yoposa, ndiyo ya Solomo.
2. Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwace;Pakuti cikondi cako ciposa vinyo.
3. Mafuta ako anunkhira bwino;Dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;Cifukwa cace anamwali akukonda.
4. Undikoke; tikuthamangire;Mfumu yandilowetsa m'zipinda zace:Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.Tidzachula cikondi cako koposa vinyo:Akukonda molungama.
5. Wakuda ine, koma wokongola,Ana akazinu a ku Yerusalemu,Ngati mahema a Kedara,Ngati nsaru zociriga za Solomo.
6. Musayang'ane pa ine, pakuti ndada,Pakuti dzuwa landidetsa.Ana amuna a amai anandikwiyira,Anandisungitsa minda yamipesa;Koma munda wanga wanga wamipesa sindinausunga.
7. Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,Umaweta kuti gulu lako?Umaligonetsa kuti pakati pa usana?Pakuti ndikhalirenji ngati wosoceraPambali pa magulu a anzako?
8. Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola,Dzituruka kukalondola bande la gululo,Nukawete ana a mbuzi zako pambali pa mahema a abusa.
9. Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe,Ngati akavalo a magareta a Farao.
10. Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi,Ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.
11. Tidzakupangira nkhata zagolidiNdi njumu zasiliva.