Numeri 26:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Moabu pa Yordano kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

4. Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israyeli, amene adaturuka m'dziko la Aigupto.

5. Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israyeli; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

6. Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.

7. Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu,

8. Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.

9. Ndi ana a Eliyabu: Nemueli, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, mula anatsutsana ndi Yehova;

Numeri 26