18. Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Cotero anandilimbitsira manja mokoma.
19. Koma Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapolo M-amoniyo, ndi Gesemu M-arabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Ciani ici mucicita? Mulikupandukira mfumu kodi?
20. Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; cifukwa cace ife akapolo ace tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena cikumbukilo, m'Yerusalemu.