Mika 7:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za colowa canu zokhala pa zokha m'nkhalango pakati pa Karimeli, zidye m'Basana ndi m'Gileadi masiku a kale lomwe.

15. Monga masiku a kuturuka kwako m'dziko la Aigupto ndidzamuonetsa zodabwitsa.

16. Amitundu adzaona nadzacita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha.

17. Adzanyambita pfumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera poturuka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa cifukwa ca iwe.

18. Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a colowa cace? sasunga mkwiyo wace ku nthawi yonse popeza akondwera naco cifundo.

19. Adzabwera, nadzaticitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zocimwa zao zonse m'nyanja yakuya,

20. Mudzapatsa kwa Yakobo coonadi, ndi kwa Abrahamu cifundo cimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.

Mika 7