20. Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wace.
21. Ndipo wina wa ophunzira ace anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga.
22. Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.
23. Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ace anamtsata Iye.
24. Ndipo onani, m panauka namondwe wamkuru panyanja, kotero kuti ngalawa inapfundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo.
25. Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tirikutayika.
26. Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikuru.
27. Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
28. Ndipo pofika Iye ku tsidya lina, ku dziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akuturuka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapa munthu pa njira imeneyo.
29. Ndipo onani, anapfuula nati, Tiri nanu ciani, inu Mwana wa Mulungu? mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yace siinafike?
30. Ndipo panali patari ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zirinkudya.
31. Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutiturutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo.
32. Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inaturuka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.
33. Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja.
34. Ndipo onani, mudzi wonse unaturukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti acoke m'malire ao.