1. Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ace;
2. ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:
3. Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4. Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.
5. Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.
6. Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.
7. Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.
8. Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.
9. Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.
10. Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
11. Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.
12. Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
13. Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14. Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.