23. Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, naciritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
24. Ndipo mbiri yace inabuka ku Suriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundu mitundu, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawaciritsa.
25. Ndipo inamtsata mipingo mipingo ya anthu ocokera ku Galileya, ndi ku Dekapole ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordano.