1. Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kumka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.
2. Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pace anamva njala.
3. Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.
4. Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa,Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akuturuka m'kamwa mwa Mulungu.
5. Pamenepo mdierekezi anamuka naye ku mzinda woyera; namuika Iye pamwamba pa cimbudzi ca Kacisi,
6. nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti,Adzauza angelo ace za iwe,Ndipo pa manja ao adzakunyamulaiwe,Ungagunde konse phazi lako pamwala.
7. Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa,Usamuyese Ambuye Mulungu wako.
8. Pomwenso mdierekezi anamuka naye ku phiri lalitari, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;