59. Ndipo ansembe akuru ndi akuru mirandu onse mafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;
60. koma sanaupeza zingakhale 2 mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pace anadza awiri,
61. nati, Uyu ananena kuti, 3 Ndikhoza kupasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu.
62. Ndipo mkuru wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Subvomera kanthu kodi? nciani ici cimene awa akunenera Iwe?
63. Koma 4 Yesu anangokhala cete. Ndipo mkuru wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.
64. Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, 5 Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.
65. Pomwepo mkuru wa ansembe 6 anang'amba zobvala zace, nati, Acitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? onani, tsopano mwamva mwanowo;
66. muganiza bwanji? lwo anayankha nati, 7 Ali woyenera kumupha,
67. 8 Pomwepo iwo anathira malobvu pankhope pace, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda kofu,
68. nati, 9 Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?
69. Ndipo 10 Petro adakhala pabwato: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.
70. Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Cimene unena sindicidziwa.
71. Ndipo pamene iye anaturuka kunka kucipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.
72. Ndipo anakananso ndi cilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo.
73. Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.
74. 11 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.
75. Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, 12 Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anaturukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.