Mateyu 26:55-69 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

55. Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munaturukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wacifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kacisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.

56. Koma izi zonse zinacitidwa, kuti 1 zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.

57. Ndipo iwo akugwira Yesu anaaka naye kwa Kayafa, mkuru wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akuru omwe.

58. Koma Petro anamtsata kutari, kufikira ku bwalo la mkuru wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone cimariziro.

59. Ndipo ansembe akuru ndi akuru mirandu onse mafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;

60. koma sanaupeza zingakhale 2 mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pace anadza awiri,

61. nati, Uyu ananena kuti, 3 Ndikhoza kupasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu.

62. Ndipo mkuru wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Subvomera kanthu kodi? nciani ici cimene awa akunenera Iwe?

63. Koma 4 Yesu anangokhala cete. Ndipo mkuru wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.

64. Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, 5 Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.

65. Pomwepo mkuru wa ansembe 6 anang'amba zobvala zace, nati, Acitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? onani, tsopano mwamva mwanowo;

66. muganiza bwanji? lwo anayankha nati, 7 Ali woyenera kumupha,

67. 8 Pomwepo iwo anathira malobvu pankhope pace, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda kofu,

68. nati, 9 Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?

69. Ndipo 10 Petro adakhala pabwato: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.

Mateyu 26