24. Mwana wa munthu acokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.
25. Ndipo Yudase, womperekayo anayankha nati, Kedi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.
26. Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ici ndi thupi langa.
27. Ndipo pamene anatenga cikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ici inu nonse,
28. pakuti ici ndici mwazi wanga wa pangano, wothiridwa cifukwa ca anthu ambiri ku kucotsa macimo.
29. Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso cipatso ici campesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa catsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.
30. Ndipo pamene anayimba nyimbo, anaturuka kunka ku phiri la Azitona.
31. Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa cifukwa ca Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa,Ndidzakantha mbusa,Ndipo zidzabalalikaNkhosa za gulu.
32. Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.
33. Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa cifukwa ca Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.
34. Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.
35. Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.
36. Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo ochedwa Getsemane, nanena kwa ophunzira ace, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.
37. Ndipo anatenga Petro ndi ana awiria Zebedayo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi cisoni ndi kuthedwa nzeru.
38. Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uti wozingidwa ndi cisoni ca kufika naco kuimfa; khalani pano mucezere pamodzi ndi Ine.
39. Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yace pansi, napemphera, nati, Atate, ngati nkutheka, cikho ici cindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma lou.
40. Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? simukhoza kucezera ndi Ine mphindi imodzi?
41. Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka.