Mateyu 24:32-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene tsopano nthambi yace iri yanthete, nipuka masa-i mba ace, muzindikira kuti dzinja liyandikira;

33. comweconso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.

34. Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kucoka, kufikira zinthu zonsezi zidzacitidwa.

35. Thambo ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai.

36. Koma za tsiku ilo ndi nthawi yace sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.

37. Ndipo 1 monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.

38. Pakuti monga m'masiku aja, cisanafike cigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'cingalawa,

39. ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira kumene cigumula cinadza, cinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.

40. Pomwepo 2 adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:

41. awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

42. 3 Cifukwa cace dikirani, pakuti simudziwa tsiku lace lakufika Ambuye wanu.

43. Koma 4 dziwani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yace ibooledwe.

44. Cifukwa cace 5 khalani inunso okonzekeratu; cifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.

45. 6 Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace anamkhazika woyang'anira banja lace, kuwapatsa zakudya pa nthawi yace?

46. Wodala kapolo amene mbuye wace, pakufika, adzampeza iye alikucita cotero.

47. Indetu, ndinena kwa inu, kuti 7 adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zace zonse.

48. Koma kapolo woipa akanena mumtima mwace, Mbuye wanga wacedwa;

Mateyu 24