Mateyu 23:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ace,

2. nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;

3. cifukwa cace zinthu ziri zonse zimene iwo akauza inu, citani nimusunge; koma musatsanza nchito zao; pakuti iwo amalankhula, komasamacita.

4. Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi cala cao.

5. Koma amacita nchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa citando cace ca njirisi zao, nakulitsa mphonje,

Mateyu 23