32. Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya cilungamo, ndipo simunamveraiye; koma amisonkho ndi akazi aciwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munaciona, simunalapa pambuyo pace, kuti mumvere iye.
33. Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
34. Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ace kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zace.
35. Ndipo olimawo anatenga akapolo ace, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.
36. Anatumizanso akapolo ena, akucuruka oposa akuyambawa; ndipo anawacitira iwo momwemo.
37. Koma pambuyo pace anatumiza kwa iwo mwana wace, nati, Adzacitira mwana wanga ulemu.
38. Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzace, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga colowa cace.
39. Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.
40. Tsono atabwera mwini munda, adzacitira olimawo ciani?
41. Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zace.
42. Yesu ananena kwa iwo, 1 Kodi simunawerenga konse m'malembo,Mwala umene anaukana omanga nyumbaWomwewu unakhala mutu wa pangondya:ici cinacokera kwa Ambuye,Ndipo ciri cozizwitsa m'maso mwathu?