12. Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, cifukwa ca Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ici acilandire.
13. Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ace pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.
14. Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: cifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.
15. Ndipo Iye anaika manja ace pa ito, nacokapo.
16. Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, cabwino nciti ndicicite, kuti ndikhale nao mayo wosatha?
17. Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za cinthu cabwino? alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
18. Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usacite cigololo, Usabe, Usacite umboni wonama,
19. Lemekeza atate wako ndi amako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
20. Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso ciani?
21. Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhaia ndi cuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
22. Koma mnyamatayo m'mene anamva conenaco, anamuka wacisoni; pakuti anali naco cuma cambiri.
23. Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ace, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini cuma adzalowa mobvutika mu Ufumu wa Kumwamba.
24. Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano, koposa mwini cuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
25. Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?
26. Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, ici sicitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
27. Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi ciani?
28. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa cimpando ca ulemerero wace, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.