21. ]
22. Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;
23. ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lacitatu. Ndipo iwo anali ndi cisoni cacikuru.
24. Ndipo pofika ku Kapernao arnene aja akulandira ndalama za kukacisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?
25. Iye anabvomera, Apereka, Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?