10. Ndipo ophunzira ace anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?
11. Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse;
12. koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwa iye, koma anamcitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo conconso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo.
13. Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi.
14. Ndipo pamene iwo anadza ku khamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati,
15. Ambuye, citirani mwana wanga cifundo; cifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawiri kawiri pamoto, ndi kawiri kawiri m'madzi.
16. Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumciritsa.
17. Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? ndidzalekerera inu nthawi yanji? mudze naye kwa Ine kuno.
18. Ndipo. Yesu anamdzudzula; ndipo ciwanda cinaturuka mwa iye; ndipo mnyamatayo anacira kuyambira nthawi yomweyo.
19. Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuciturutsa?
20. Ndipo Iye ananena kwa iwo, Cifukwa cikhulupiriro canu ncacing'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala naco cikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosacitika. [