Mateyu 16:22-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzicitireni cifundo, Ambuye; sicidzatero kwa Inu ai.

23. Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe condikhumudwitsa Ine; cifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.

24. Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine.

25. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa ca Ine, adzaupeza.

26. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wace? kapena munthu adzaperekanji cosintha ndi moyo wace?

Mateyu 16