1. Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse cizindikiro ca Kumwamba.
2. Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwe; popeza thambo liri laceza.
3. Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo; popeza thambo liri la ceza codera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yin o, simungathe kuzindikira.
4. Obadwa oipa ndi acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sadzalandira cizindikiro cina, koma cizindikiro ca Yona. Ndipo Iye anawasiya, nacokapo.
5. Ndipo ophunzira anadza ku tsidya linalo, naiwala kutenga mikate.
6. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi ndi Asaduki.
7. Ndipo iwo anafunsana wina ndi mnzace, nati, Sitinatenga mikate.
8. Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana cifukwa ninji wina ndi mnzace, kuti simunatenga mikate?
9. kodi cikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi mitanga ingati munaitola?
10. Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi malicero angati munawatola?
11. Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani cotupitsa ca Afarisi ndi Asaduki.
12. Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauza kupewa cotupitsa ca mikate, koma ciphunzitso ca Afarisi ndi Asaduki.
13. Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kaisareya wa Filipi, anafunsa ophunzira ace, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani?
14. Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.