Mateyu 15:20-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthuai.

21. Ndipo Yesu anaturukapo napatukira ku mbali za Turo ndi Sidoni.

22. Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anaturuka m'malire, napfuula, nati, Mundicitire ine cifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi ciwanda.

23. Koma Iye sanamyankha mau amodzi. Ndipo ophunzira ace anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti apfuula pambuyo pathu.

24. Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israyeli.

25. Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine.

26. Ndipo Iye anayankha, nati, Sicabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagaru.

27. Koma iye anati, Etu, Ambuye, pakutinso tiagaru timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.

28. Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, cikhulupiriro cako ndi cacikuru; cikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wace anacira nthawi yomweyo.

29. Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.

30. Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ace: ndipo Iye anawaciritsa;

Mateyu 15