Mateyu 13:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsiku lomwelo Yesu anaturuka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja.

2. Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.

3. Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anaturuka kukafesa mbeu,

4. Ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo.

5. Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya, Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera;

6. ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.

7. Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo.

8. Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.

9. Amene ali ndi makutu, amve.

10. Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?

Mateyu 13