Mateyu 12:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Afarisi anaturuka, nakhala upo womcitira Iye mwa kumuononga.

15. Koma Yesu m'mene anadziwa, anacokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawaciritsa iwo onse,

16. nawalimbitsira mau kuti asamuulule Iye;

17. kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri uja, kuti,

18. Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha,Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye;Pa Iye ndidzaika Mzimu wanga,Ndipo Iye adzalalikira ciweruzo kwa akunja.

19. Sadzalimbana, sadzapfuula;Ngakhale mmodzi sadzamva mau ace m'makwalala;

20. Bango lophwanyika sadzalityola,Ndi nyali yofuka sadzaizima,Kufikira Iye adzatumiza ciweruzo cikagonjetse,

21. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lace.

22. Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi ciwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamciritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.

23. Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?

24. Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samaturutsa ziwanda koma ndi mphamvu yace ya Beelzebule, mkuru wa ziwanda.

Mateyu 12