1. Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ace anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.
2. Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu acita cosaloleka tsiku la Sabata.
3. Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenga cimene anacicita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?
4. kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okha okha.
5. Kapena simunawerenga kodi m'cilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m'Kacisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda cimo?
6. Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kacisiyo ali pompano.
7. Koma mukadadziwa nciani ici:Ndifuna cifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osacimwa,
8. pakuti Mwana wa munthu ali mwini tsiku la Sabata.
9. Ndipo Iye anacokera pamenepo, nalowa m'sunagoge mwao;
10. ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala, Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuciritsa tsiku la Sabata? kuti ampalamulitse mlandu.