2. Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende nchito za Kristu, anatumiza ophunzira ace mau,
3. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?
4. Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:
5. akhungu alandira kuona kwao, Ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, indi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino.