11. Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;Munthu adzandicitanji?
12. Zowindira Inu Mulungu, ziri pa ine:Ndidzakucitirani zoyamika.
13. Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa:Simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?Kuti ndiyende pamaso pa MulunguM'kuunika kwa amoyo.