Marko 9:45-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m'moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m'gehena.[

46. ]

47. Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'gehena;

48. kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi mota suzimidwa.

49. Pakuti onse adzathiridwa mcere wamoto,

50. Mcere uli wabwino; koma ngati mcere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi ciani? Khalani nao mcere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzace.

Marko 9