Marko 15:42-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata,

43. anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.

44. Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.

45. Ndipo pamene anacidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe ntembowo.

46. Ndipo anagula oafuta, namtsitsa Iye, namkulunga n'bafutamo, namuika m'manda osenedwa m'thanthwe; nakunkhunicira mwala pa khomo la manda.

47. Ndipo Maliya wa Magadala ndi Maliya amace wa Yose anapenya pomwe anaikidwapo.

Marko 15