41. amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.
42. Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata,
43. anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.
44. Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.
45. Ndipo pamene anacidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe ntembowo.