Maliro 2:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira;Wapereka m'manja a adani ace makoma a zinyumba zace;Iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

8. Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni;Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo;Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

9. Zipata zace zalowa pansi; waononga ndi kutyola mipiringidzo yace;Mfumu yace ndi akalonga ace ali pakati pa amitundu akusowa cilamulo;Inde, aneneri ace samalandira masomphenya kwa Yehova.

10. Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m'cuuno mwao:Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.

11. Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.

Maliro 2