12. Koma m'mene Petro anaciona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi cipembedzo cathu?
13. Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wace Yesu; amene, inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.
14. Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,