10. namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kacisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ici cidamgwera.
11. Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse ku khumbi lochedwa la Solomo, alikudabwa ndithu.
12. Koma m'mene Petro anaciona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi cipembedzo cathu?
13. Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wace Yesu; amene, inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.
14. Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,
15. ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ici ife tiri mboni.
16. Ndipo pa cikhulupiriro ca m'dzina lace dzina lacelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo cikhulupiriro ciri mwa iye cinampatsa kucira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.
17. Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti munacicita mosadziwa, monganso akulu anu.
18. Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Kristu, iye anakwaniritsa cotero.