10. Koma Paulo anati, ndirikuimirira pa mpando waciweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawacitira-kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.
11. Pamenepo ngati ndiri wocita zoipa, ngati ndacita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zacabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditurukira kwa Kaisara.
12. Pamenepo Festo, atakamba ndi aphungu ace, anayankha, Wanena, Ndirurukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.
13. Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bemike anafika ku Kaisareya, nalankhula Festo.
14. Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festo anafotokozera mfumuyo mlandu wace wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felike,