Macitidwe 2:27-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Hade,Kapena simudzapereka Woyera wanu aone cibvunde,

28. Munandidziwitsa ine njira za moyo;Mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.

29. Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davine, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ace ali ndi ife kufikira lero lino.

30. Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi Iumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa cipatso ca m'cuuno mwace adzakhazika wina pa mpando wacifumu wace;

Macitidwe 2